Kugwiritsa ntchito ndalama moyipa

Ndime izi zimaonetsa mmene ndalama zimaipitsira anthu, zitakhala chifukwa cha kupereka munthu, kuyesa kuwononga mtundu wonse ndi kupha anthu.

Kuperekedwa kwa Yesu

Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. (Mateyu 26:14-15)
Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu. Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.” Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.” Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira. Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.” Choncho anagwirizana kuti ndalamazo azigwiritse ntchito pogulira munda wa wowumba mbiya kuti ukhale manda alendo. Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino. Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli. Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.” (Mateyu 27:3-10)
Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke. (Marko 14:10-11)
Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. (Luka 22:3-5)
(Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka. (Machitidwe a Atumwi 1:18)

Abale ogulitsidwa kukhala akapolo

Amalonda ena a ku Midiyani ankadutsa pomwepo. Tsono abale ake a Yosefe anamutulutsa Yosefe uja mu chitsime chija ndipo anamugulitsa kwa Aismaeli aja pamtengo wa masekeli makumi awiri. Choncho anapita naye Yosefe ku Igupto. (Genesis 37:28)

Ndalama zolipira ula

Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena. (Numeri 22:7)
Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga. (Numeri 22:18)
...kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? (Numeri 24:13)

Ndalama zoperekedwa kuti ayese kuwononga mtundu wa Ayuda

Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.” Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.” (Estere 3:9-11)
Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda. (Estere 4:7)

Ndalama zolipira kuti avulaze Samsoni

Pambuyo pake, Samsoni anayamba kukonda mtsikana wina wa ku chigwa cha Soreki dzina lake Delila. Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.” (Oweruza 16:4-5)
Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo. (Oweruza 16:18)

Ndalama zolipira kupha munthu

Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira. (Oweruza 9:4)