Msonkho

Kulipira msonkho ndi lamulo la Baibulo, lotsimikiziridwa ndi Yesu ndi mtumwi Paulo, limene limavomereza ulamuliro wa boma. Zitsanzo mʼMalemba onse zimaonetsa mfundo imeneyi, ndipo zimaonetsanso nthawi zina pamene panali zosiyana.

Ambuye alibe tsankho

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. (Deuteronomo 10:17)
Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.” (2 Mbiri 19:7)
Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake? (Yobu 34:19)
Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. (Aefeso 6:9)

Sitiyenera kukhala ndi tsankho

Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi. (Miyambo 28:21)

Tsankho ndi tchimo

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. (Yakobo 2:8-9)

Usakondere wolemera

Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa? Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa? Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. (Yakobo 2:1-9)

Usakondere wosauka

Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere. (Eksodo 23:3)
“ ‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo. (Levitiko 19:15)

Atsogoleri/oweruza sayenera kukhala ndi tsankho

Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.” (Deuteronomo 1:17)
Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. (Deuteronomo 16:18-19)
Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.” (2 Mbiri 19:6-7)

Wotembereredwa ngati ali ndi tsankho

“Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.” (Malaki 2:9)

Maganizo oyenera

Khalani ndi maganizo amodzi wina ndi mnzake

Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse. (Aroma 12:16)

Ganizirani ena kukhala ofunika kuposa inu

Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. (Afilipi 2:3)