Lamulo losapondereza osauka
“Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto. “Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo. Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo. (Eksodo 22:21-24)
Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake, kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo. (Yobu 34:28)
Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda. (Miyambo 28:3)
Oyipa amapondereza osauka
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi. Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona. (Yesaya 32:6-7)
Kufotokozera anthu amene amapondereza osauka
Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka. (Miyambo 28:15)
Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi. Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.” (Miyambo 30:14)
Chiweruzo pa amene amapondereza osauka
Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka; (Yobu 20:10)
Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo. (Yobu 20:15)
Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake. Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange. “Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho. (Yobu 20:18-20)
...mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake. (Yobu 20:26)
Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu. (Yobu 20:28)
Oyipa amasolola lupanga ndi kupinda uta kugwetsa osauka ndi osowa, kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama. Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka. (Masalimo 37:14-15)
Wokongoza alande zonse zimene ali nazo; alendo afunkhe ntchito za manja ake. (Masalimo 109:11)
Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima. (Masalimo 109:16)
Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka. (Miyambo 22:16)
Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu, pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo. (Miyambo 22:22-23)
Yehova akuwazenga milandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake: “Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa; nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi. Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga, nʼkudyera masuku pamutu amphawi?” Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse. (Yesaya 3:14-15)
Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo, kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye. (Yesaya 10:1-2)
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ” (Yeremiya 22:1-5)
Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye. (Ezekieli 22:7)
Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo. (Ezekieli 22:29)
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva, ndi osauka ndi nsapato. Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera. (Amosi 2:6-7)
Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya, inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!” Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti, “Nthawi idzafika ndithu pamene adzakukokani ndi ngowe, womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza. (Amosi 4:1-2)
Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa), inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona. Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake. Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu. (Amosi 5:9-12)
Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu. Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo, tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?” (Amosi 8:4-6)
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’ “Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri. (Zekariya 7:9-12)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.” (Malaki 3:5)
Pempho kuti Ambuye aweruze kuponderezedwa kwa osauka
Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera. (Masalimo 94:2)
Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye. (Masalimo 94:6)
Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.” (Masalimo 94:7)
Chitsanzo cha kupondereza osauka
Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi, (Yeremiya 2:34)
Anthu opembedza amene amapondereza osauka
Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.” (Marko 12:38-40)
“Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando. Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.” (Luka 20:46-47)
Kupondereza osauka nʼkofala
Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa. (Mlaliki 5:8)
Teteza/thandiza osauka/osowa thandizo
Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera. Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka. (Miyambo 31:8-9)
...phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.” (Yesaya 1:17)
...inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti, “ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse; pulumutsani mʼdzanja la wozunza aliyense amene walandidwa katundu wake, kuopa kuti ukali wanga ungabuke ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika chifukwa cha zoyipa zimene mwachita. (Yeremiya 21:12)
Anthu opembedza amathandiza osauka
Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi. (Miyambo 29:7)
Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka? (Yobu 30:25)
Ambuye amadalitsa amene amathandiza osauka
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake. Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda. (Masalimo 41:1-3)
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere. (Miyambo 19:17)
Anadalitsa mtsogoleri amene anathandiza osauka
Ngati mfumu iweruza osauka moyenera, mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse. (Miyambo 29:14)
Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu. “Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, (Yeremiya 7:5-9)
Dyetsa osauka ndipo Ambuye adzakubwezera
Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.” Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.” Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri. Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’ “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’ “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’ “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’ “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’ “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze. (Luka 14:12-23)
Weruza wosauka mwachilungamo
“Usakhotetse milandu ya anthu osauka. (Eksodo 23:6)
Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole. (Deuteronomo 24:17)
Chitira chifundo osauka
Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna. Lamulo losiya tsinde la mtengo ndi mizu yake litanthauza kuti ufumu wanu udzabwezeredwa kwa inu mukadzavomereza kuti Mulungu ndiye amalamulira. Nʼchifukwa chake mfumu, chikukomereni kulandira malangizo anga: Lekani machimo ndipo muzichita zabwino, lekani mphulupulu zanu ndipo muzikomera mtima anthu opsinjika. Nʼkutheka kuti mtendere wanu udzapitirira.” (Danieli 4:25-27)
Amene sateteza osauka adzaweruzidwa
Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo ngati zikwere zodzaza ndi mbalame. Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera. Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala. Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire; saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino, sateteza ufulu wa anthu osauka. Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi? Kodi ndisawulipsire mtundu woterewu? Akutero Yehova. (Yeremiya 5:27-29)
Tchimo la Sodomu: kusathandiza osauka
“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. (Ezekieli 16:49)
Chitsanzo cha mtsogoleri amene sanateteze osauka
Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye. (Yesaya 1:23)
Mmene timachitira ndi osauka zimaonetsa za Ambuye
Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu. (Miyambo 14:31)
Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa. (Miyambo 17:5)
Gawo la Mulungu kwa osauka
Ambuye amapereka/amateteza osauka ndi osowa
Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. (Deuteronomo 10:18)
Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu. (Yobu 5:15)
Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse. (Masalimo 9:18)
Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye. (Masalimo 10:14)
“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.” (Masalimo 12:5)
Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse. (Masalimo 34:6)
Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.” (Masalimo 35:10)
Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe. (Masalimo 40:17)
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi. (Masalimo 68:6)
Anthu anu anakhala mʼmenemo ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu. (Masalimo 68:10)
Yehova amamvera anthu osowa ndipo sanyoza anthu ake omangidwa. (Masalimo 69:33)
Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo. (Masalimo 102:17)
Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu, osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako. (Masalimo 107:4)
Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo, kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa. (Masalimo 109:31)
Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala; (Masalimo 113:7)
Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri; anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya. (Masalimo 132:15)
Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa. (Masalimo 140:12)
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende, (Masalimo 146:7)
Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa. (Masalimo 146:9)
Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa. (Masalimo 147:6)
Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye. (Miyambo 15:25)
...koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa. (Yesaya 11:4)
Osaukitsitsa adzapeza chakudya ndipo amphawi adzakhala mwamtendere. Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala, ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako. (Yesaya 14:30)
Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka, mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake. Mwakhala ngati pobisalirapo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa. Pakuti anthu ankhanza ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma, (Yesaya 25:4)
“Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza; ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu. Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo; Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya. (Yesaya 41:17)
Imbirani Yehova! Mutamandeni Yehova! Iye amapulumutsa wosauka mʼmanja mwa anthu oyipa. (Yeremiya 20:13)
Pemphero kuti Ambuye athandize osauka
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo. Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo. Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza. Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa. Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake. Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse. (Masalimo 72:4, 10, 12-15)
Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi; osauka ndi osowa atamande dzina lanu. (Masalimo 74:21)
Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. (Masalimo 82:3-4)
Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse, muchite nane molingana ndi dzina lanu, chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni. Pakuti ndine wosauka ndi wosowa, ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga. (Masalimo 109:21-22)
Maganizo a anthu pa gawo la Mulungu ndi osauka
Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba. Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole. Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko. Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo. Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa. Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda. Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo. Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole. Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala. Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa; amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu. Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense. Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala. (Yobu 24:2-12, 14)
Maganizo a Mulungu pa osauka
Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. (Chivumbulutso 2:9)
Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone. (Chivumbulutso 3:17-18)
Ambuye anasankha ofowoka kuti achititse manyazi amphamvu
Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. (1 Akorinto 1:26-27)
Ambuye analenga anthu onse
Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova. (Miyambo 22:2)
Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti: Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa. (Miyambo 29:13)
Maganizo a anthu pa osauka
Kodi munthu wanzeru amaposa motani chitsiru? Kodi munthu wosauka amapindula chiyani podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena? (Mlaliki 6:8)
Mavuto ndi ubwino kwa osauka
Mavuto a osauka
Osauka ali ndi abwenzi ochepa
Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri. (Miyambo 14:20)
Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa. (Miyambo 19:4)
Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo adzamuthawa kupita kutali. Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse. (Miyambo 19:7)
Osauka amazunzidwa ndi kupanda chilungamo
Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amachilanda. (Miyambo 13:23)
Osauka amalankhula ndi olemera modzichepetsa
Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali. (Miyambo 18:23)
Osauka amatumikira olemera
Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo. (Miyambo 22:7)
Osauka amanyalanyazidwa
Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake. (Mlaliki 9:14-16)
Umphawi
Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka. (Miyambo 10:15)
Pemphero losakhala wosauka
“Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri musandimane zimenezo ndisanafe: Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.” (Miyambo 30:7-9)
Ubwino kwa osauka
Osauka amatchedwa odala
Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu. (Luka 6:20)
“Ndinu atsoka, anthu olemera, popeza mwalandiriratu zokusangalatsani. (Luka 6:24)
Osauka ndi olemera mʼchikhulupiriro
Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? (Yakobo 2:5)
Osauka amalalikidwa uthenga wabwino
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende. (Yesaya 61:1)
Yohane ali mʼndende anamva zimene Khristu ankachita, ndipo anatumiza ophunzira ake kukamufunsa Iye. Anamufunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankanena kuti mudzabwerayu kapena tidikire wina?” Yesu anayankha kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwamva ndi kuona. Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. (Mateyu 11:2-5)
“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa, (Luka 4:18)
Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. (Luka 7:22)
Osauka sadzabedwa chifukwa cha chuma
Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo. (Miyambo 13:8)
Osauka amene amadziwa Ambuye adzatonthozedwa kumwamba
“Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake. “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’ “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. (Luka 16:19-25)
Osauka akhoza kunyadira ngati ana a Mulungu
Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. (Yakobo 1:9-10)
Pa kubwezeretsedwa kwa Israeli, osauka adzapindula
Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova; ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli. (Yesaya 29:19)
Wosauka koma wanzeru amazindikira wolemera
Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira. (Miyambo 28:11)
Zinthu zimene umphawi umaziposa
Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota. (Miyambo 19:1)
Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza. (Miyambo 19:22)
Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota. (Miyambo 28:6)
Zitsanzo za osauka
Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.” (1 Samueli 18:23)
Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe. (Masalimo 70:5)
Pemphero la Davide. Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosowa. (Masalimo 86:1)
Anthu ake onse akubuwula pamene akufunafuna chakudya; asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. “Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani, chifukwa ine ndanyozeka.” (Maliro 1:11)
Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.” (Luka 2:22-24)
Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. (1 Akorinto 4:11-12)
Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse. (2 Akorinto 6:4-5, 10)
Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. (2 Akorinto 11:27)
Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. (Afilipi 4:11-14)
Osauka/olemera mu mpingo
Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni. (1 Akorinto 11:18-22)
Kupereka kwa osauka
Kubwezeredwa kwa dziko
Kwa inu chakachi chidzakhaladi chaka choyimba lipenga kukondwerera zaka makumi asanu. Pa chaka chimenechi musadzale kanthu ndipo musakolole mbewu zomera zokha kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosasadzira. Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Choncho chikhale chaka chopatulika kwa inu. Muzidya zokhazo zimene zakololedwa mʼminda. “ ‘Chaka chimenechi ndi choliza lipenga, kukondwerera zaka makumi asanu, ndipo aliyense abwerere pa malo ake. (Levitiko 25:11-13)
Malamulo okhudza osauka amene anakhala akapolo
“ ‘Ngati mʼbale wanu asauka ndipo adzigulitsa yekha kwa inu, musamugwiritse ntchito ngati kapolo. Akhale ngati wantchito kapena ngati mlendo. Akugwirireni ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Kenaka iye ndi ana ake achoke, ndipo apite ku fuko lake ndi kubwerera ku malo a makolo ake. Chifukwa Aisraeli ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto, asagulitsidwe ngati akapolo. Musawalamulire mwankhanza koma wopani Mulungu wanu. “ ‘Kunena za akapolo aamuna ndi aakazi, amenewa mungathe kuwagula kuchokera kwa mitundu ya anthu imene yakuzungulirani. Mungathenso kugula akapolo kuchokera kwa alendo amene akukhala nanu kapena kuchokera ku mabanja amene mukukhala nawo amene ndi mbadwa za mʼdziko lanu. Iwowa akhoza kukhala akapolo anu. Akapolowo mungathe kuwasiya mʼmanja mwa ana anu inu mutafa kuti akhale cholowa chawo moyo wawo wonse. Koma musawalamulire mwankhanza Aisraeli anzanu. “ ‘Ngati mlendo kapena munthu amene akukhala nanu kwa kanthawi kochepa alemera ndipo mmodzi wa abale anu amene akukhala naye pafupi nʼkusauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendo amene akukhala pakati panuyo kapena kwa mmodzi wa fuko la munthu wongokhala pafupi nayeyo, wodzigulitsayo ali ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola: amalume ake kapena mwana wa amalume ake, kapena wachibale wa mu fuko lake. Kapena ngati iye mwini alemera, atha kudziwombola yekha. Iye pamodzi ndi munthu amene anamugulayo awerengerane kuyambira chaka chimene anadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Mtengo wodziwombolera ukhale wofanana ndi zakazo. Ndipo nthawi imene anali ndi mbuye wakeyo iwerengedwe ngati nthawi ya munthu wantchito. Ngati patsala zaka zambiri, iye ayenera kulipira mtengo woposera umene anamugulira. Ngati kwatsala zaka zochepa kuti ifike nthawi ya chaka chokondwerera zaka makumi asanu, iye awerengerane ndi mbuye wake, ndipo apereke ndalama za zowomboledwera molingana ndi zaka zotsalazo. Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa chaka ndi chaka. Ndipo muonetsetse kuti mbuye wakeyo sakumulamulira mwankhanza. “ ‘Ngakhale munthuyo atapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, iye ndi ana ake ayenera kumasulidwa mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu, (Levitiko 25:39-54)
Kusamvera malamulo kunabweretsa chiweruzo
“Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati, ‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse. Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi. Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu. “Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. (Yeremiya 34:13-17)
Zina ndi zina
Zinthu zimene zimapangitsa munthu kukhala wosauka
Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa, koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa. (Miyambo 13:18)
Usakonde tulo ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri. (Miyambo 20:13)
Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. (Miyambo 21:17)
Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera. Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza. (Miyambo 23:20-21)
Sipakanakhala wosauka mʼdziko ngati anthu akanamvera kwathunthu
Komabe pasadzakhale wosauka pakati panu chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani kwambiri mʼdziko limene adzakupatsani kuti likhale lanu ngati cholowa chanu. Adzakudalitsani pokhapokha ngati mudzamveradi Yehova Mulungu wanu posunga ndi kutsatira malamulo onse amene ndikukupatsani lero. (Deuteronomo 15:4-5)
Osauka okha ndiwo anatsala mʼdziko logonjetsedwa
Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo. (2 Mafumu 24:14)
Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina. (2 Mafumu 25:12)
Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso. (Yeremiya 39:10)
Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni. (Yeremiya 40:7)
Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. (Yeremiya 52:15)