Maganizo a Baibulo pa chuma
Maganizo a Ambuye pa chuma
Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. (Chivumbulutso 2:9)
Maganizo a anthu pa chuma
Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake. (Yobu 5:5)
Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa, ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi. (Yobu 15:29)
Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka; (Yobu 20:10)
Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo. (Yobu 20:15)
Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake. Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange. “Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho. (Yobu 20:18-20)
...mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake. (Yobu 20:26)
Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu. (Yobu 20:28)
Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere. (Yobu 21:13)
Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa. (Yobu 21:16)
Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa; ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako, ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi, golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa. Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali. (Yobu 22:23-25)
“Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa, cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse. (Yobu 27:13)
Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, ndi kukundika zovala ngati mchenga, zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale, ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo. (Yobu 27:16-17)
Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira, adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere, adzatsiriza zaka zawo mosangalala. (Yobu 36:11)
Kodi chuma chanu kapena mphamvu zanu zonse zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso? (Yobu 36:19)
Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano. Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo. (Mlaliki 7:11-12)
Sitimatenga kanthu tikamwalira
Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira; Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye. Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino, iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala. Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo. (Masalimo 49:16-20)
Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano: chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe, kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka, kotero kuti pamene wabereka mwana alibe kanthu koti amusiyire. Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake, ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho. Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake. (Mlaliki 5:13-15)
Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. (1 Timoteyo 6:7)
Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku: Iye amangovutika koma popanda phindu; amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani. (Masalimo 39:6)
Sungathe kugula chiwombolo cha moyo wako
Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira. Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo? Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu. Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire, (Masalimo 49:5-8)
Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. (Miyambo 11:4)
Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? (Mateyu 16:26)
Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? (Marko 8:36-37)
Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? (Luka 9:25)
Chuma chimabweretsa “abwenzi” ambiri
Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri. (Miyambo 14:20)
Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa. (Miyambo 19:4)
Chuma sichikhalitsa
Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa. Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga. (Miyambo 23:4-5)
Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. (Ahebri 11:24-26)
Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. (1 Petro 1:7)
Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. (1 Petro 1:18)
Chuma chonse si kanthu poyerekeza ndi kudziwa Yesu
Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu (Afilipi 3:7-8)
Chuma nʼchosadalirika
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. (1 Timoteyo 6:17)
Chuma nʼchopanda phindu popanda Ambuye
Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane. Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna; mtima wanga sindinawumane zokondweretsa. Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse, ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa. Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga, ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze, zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe, palibe chomwe ndinapindula pansi pano. (Mlaliki 2:4-11)
Zinthu zamtengo wapatali kuposa chuma
Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri, mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri. Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri, kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro. Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi, sungayigule ndi zokometsera zagolide. Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe; mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi. Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi; nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri. (Yobu 28:15-19)
Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri; (Masalimo 37:16)
Ndimakondwera potsatira malamulo anu monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri. (Masalimo 119:14)
Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide. (Masalimo 119:72)
Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino, (Masalimo 119:127)
Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru. Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu. (Miyambo 3:13-16)
Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino. Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru. (Miyambo 8:10-11)
Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika. Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri. Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo. Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma. (Miyambo 8:18-21)
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto. (Miyambo 15:16)
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo. (Miyambo 16:8)
Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva. (Miyambo 16:16)
Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada. (Miyambo 16:19)
Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota. (Miyambo 19:1)
Pali golide ndi miyala yamtengowapatali, koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi. (Miyambo 20:15)
Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri; kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide. (Miyambo 22:1)
Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota. (Miyambo 28:6)
Kwa amene anapatsidwa zambiri adzafunsidwa zambiri
Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.” (Luka 12:48)
Madalitso a chuma
Olungama adzalandira mphotho ya kulemera
Choyipa chitsata mwini, koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino. (Miyambo 13:21)
Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto. (Miyambo 15:6)
Chuma kwa munthu amene amasinkhasinkha Mawu a Mulungu
Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho. (Masalimo 1:1-3)
Olemera adzapembedza Ambuye
Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo. (Masalimo 22:29)
Kupempherera kulemera
...kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika, kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani. (Masalimo 106:5)
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino. Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.” (Masalimo 122:6-7)
Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, (Masalimo 128:5)
Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu. (3 Yohane 2)
Anthu olemera opembedza
Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. (Genesis 12:5)
Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide. (Genesis 13:2)
Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. Koma ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo ndipo pambuyo pake iwo adzatulukamo ndi chuma chambiri. (Genesis 15:13-14)
Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita. (Genesis 24:1)
Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda. (Genesis 24:16)
Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu. (Genesis 24:35)
Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa. Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje. (Genesis 26:12-14)
Mwa njira imeneyi, Yakobo analemera kwambiri ndipo anali ndi ziweto zochuluka kwambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamira ndi abulu. (Genesis 30:43)
Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira. (Genesis 33:11)
Ndipo Farao anavula mphete ku chala chake nayiveka ku chala cha Yosefe. Anamuvekanso mkanjo wonyezimira ndi nkufu wagolide mʼkhosi mwake. (Genesis 41:42)
Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.” (Genesis 45:13)
Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto. (Genesis 46:6)
Tsono Aisraeli anakhazikika mʼdziko la Igupto ku chigawo cha Goseni. Kumeneko anapeza chuma ndipo anaberekana nachuluka kwambiri. (Genesis 47:27)
...nawawuza kuti, “Mukubwerera kwanu ndi chuma chambiri. Muli ndi ngʼombe zambiri pamodzi ndi siliva, golide, mkuwa ndi chitsulo, ndiponso zovala zambiri. Izi zimene munafunkha kwa adani anu agawireni abale anu.” (Yoswa 22:8)
Naomi anali ndi mʼbale wake wolemera kwambiri wochokera ku banja la mwamuna wake Elimeleki, dzina lake Bowazi. (Rute 2:1)
“Inu ana aakazi a Israeli, mulireni Sauli, amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa, amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide. (2 Samueli 1:24)
Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga, Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva. (1 Mafumu 10:4, 7)
Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. (1 Mafumu 3:11-13)
Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera. (1 Mbiri 29:23)
Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. (1 Mbiri 29:28)
Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo, Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.” (2 Mbiri 1:11-12)
Mfumu Solomoni anapambana mafumu ena onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. (2 Mbiri 9:22)
Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri. (2 Mbiri 17:5)
Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700. Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda (2 Mbiri 17:11-12)
Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu. (2 Mbiri 18:1)
Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali. Iye anamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta a olivi, ndiponso anamanga nyumba zodyeramo ngʼombe zosiyanasiyana, ndi makola a nkhosa. Iyeyo anamanga midzi ndipo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, pakuti Mulungu anamupatsa chuma chambiri. Ndi Hezekiya amene anatseka ku mtunda kwa kasupe wa Gihoni, ndi kumuwongolera kuti madzi ake apite mbali ya kumadzulo kwa Mzinda wa Davide. Iye ankachita bwino pa ntchito iliyonse imene ankagwira. (2 Mbiri 32:27-30)
Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana. (Nehemiya 9:25)
...ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa. (Yobu 1:3)
Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni. (Danieli 3:30)
Pamene kumada, kunabwera munthu wolemera wa ku Arimateyu dzina lake Yosefe amene anali wophunzira wa Yesu. (Mateyu 27:57)
Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. (1 Akorinto 4:8, 11-12)
Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. (Afilipi 4:11-18)
Ambuye amakondwera ndi kulemera kwa atumiki ake
Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa, afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo. Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke, Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.” (Masalimo 35:27)
Si onse amene adzalemera
Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje. Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa. Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife. (Ahebri 11:36-40)
Yesu ndi woyenera kulandira chuma
Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti, “Mwana Wankhosa amene anaphedwayu ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi mayamiko.” (Chivumbulutso 5:12)
Anthu anzeru akhoza kulemera
Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe, koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru. (Miyambo 14:24)
Mmene chuma chimapezekera
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu; Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino. (Miyambo 24:3-4)
Zinthu zimene zimalepheretsa anthu kulemera
Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. (Miyambo 21:17)
Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka. (Miyambo 22:16)
Zoopsa za chuma
Kukonda chuma
Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho. (Masalimo 62:10)
Kunyada
Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako unadzipezera chuma ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zosungira chuma chako. Ndi nzeru zako zochitira malonda unachulukitsa chuma chako ndipo wayamba kunyada chifukwa cha chuma chakocho. (Ezekieli 28:4-5)
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. (1 Timoteyo 6:17)
Olemera sayenera kunyada chifukwa moyo ndi waufupi
Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake. (Yakobo 1:9-11)
Nyadira mwa Ambuye, osati mu chuma
Yehova akuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake, kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake, koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi: kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa, kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo, chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi. Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,” akutero Yehova. (Yeremiya 9:23-24)
Chuma chimapereka maganizo a chitetezo
Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka. (Miyambo 10:15)
Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba; chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza. (Miyambo 18:11)
Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.” Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima. (Masalimo 30:6-7)
Amene amadalira chuma
Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena. Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo. Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama. (Masalimo 49:10-12)
Chuma chimakonda kulekanitsa anthu
Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi. Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo. Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.” Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. (Genesis 13:5-11)
Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa. Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje. Nthawi iyi nʼkuti Afilisti atakwirira ndi dothi zitsime zonse zimene antchito abambo ake Abrahamu anakumba mu nthawi ya abambo akewo. Ndipo Abimeleki anati kwa Isake, “Muchoke pakati pathu chifukwa mwasanduka wamphamvu kuposa ife.” (Genesis 26:12-16)
Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. (Genesis 36:6-7)
Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba, ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda, mpaka mutalanda malo onse kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo. (Yesaya 5:8)
Chuma chingathe kulekanitsa Akhristu
Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni. (1 Akorinto 11:18-22)
Chuma ndi chonyenga/chingathe kutsamwitsa kubereka zipatso
Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni. (Miyambo 11:18)
Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. (Mateyu 13:4-5, 7, 22)
Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. (Marko 4:2-3, 7, 18-19)
Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. (Luka 8:7, 14)
Nʼkovuta kuti wolemera alowe mu Ufumu
Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?” Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.” Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?” Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.” Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?” Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri. Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.” Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?” Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.” (Mateyu 19:16-26)
Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ” Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.” Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.” Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri. Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!” Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.” Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?” Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.” (Marko 10:17-27)
Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!” Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.” (Luka 18:28-30)
Olemera amene sadziwa Ambuye adzalekanitsidwa naye kwamuyaya
“Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake. “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’ “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. (Luka 16:19-25)
Olemera amaganiza kuti ndi anzeru
Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira. (Miyambo 28:11)
Mmene olemera amachitira ndi osauka
Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali. (Miyambo 18:23)
Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo. (Miyambo 22:7)
Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa? (Yakobo 2:6-7)
Chuma chingapangitse anthu kuyiwala Ambuye
Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo. (Deuteronomo 6:10-12)
...dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa. Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani. Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino. (Deuteronomo 8:9-18)
Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa. (Deuteronomo 31:20)
“Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri musandimane zimenezo ndisanafe: Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.” (Miyambo 30:7-9)
Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere. Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’ Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono. Simunandimvere Ine. Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo. Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa chifukwa cha zoyipa zanu zonse. (Yeremiya 22:21-22)
Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone. (Chivumbulutso 3:17-18)
Chuma chimayambitsa nsanje
Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa. Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje. (Genesis 26:12-14)
Ndipo Abimeleki anati kwa Isake, “Muchoke pakati pathu chifukwa mwasanduka wamphamvu kuposa ife.” (Genesis 26:16)
Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani ankanena kuti, “Yakobo watenga chilichonse cha abambo athu ndipo wapeza chuma chonsechi pogwiritsa ntchito chuma cha abambo athu.” (Genesis 31:1)
Matemberero a chuma
Temberero la kubedwa
Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo. (Miyambo 13:8)
Temberero la kusowa tulo
Wantchito amagona tulo tabwino ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri, koma munthu wolemera, chuma sichimulola kuti agone. (Mlaliki 5:12)
Tsoka limene linalengezedwa kwa olemera
“Ndinu atsoka, anthu olemera, popeza mwalandiriratu zokusangalatsani. (Luka 6:24)
Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza. Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa. (Yakobo 5:1-5)
Nʼchifukwa chiyani oyipa amalemera?
Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake; amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova. Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu; mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu. Zinthu zake zimamuyendera bwino; iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali; amanyogodola adani ake onse. (Masalimo 10:3-5)
Salimo la Davide. Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa; pakuti monga udzu iwo adzafota msanga, ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga. Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa. Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa, koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko. Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso; ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso. Koma ofatsa adzalandira dziko ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu. (Masalimo 37:1-2, 7, 9-11)
Salimo la Asafu. Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli, kwa iwo amene ndi oyera mtima. Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka; ndinatsala pangʼono kugwa. Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira, pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa. Iwo alibe zosautsa; matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu. Saona mavuto monga anthu ena; sazunzika ngati anthu ena onse. Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo; amadziveka chiwawa. Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa; zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire. Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa; mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.” Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi. Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo ndi kumwa madzi mochuluka. Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji? Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?” Umu ndi mmene oyipa alili; nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira. Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera; pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga. Tsiku lonse ndapeza mavuto; ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse. Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,” ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu. Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi, zinandisautsa kwambiri kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu; pamenepo ndinamvetsa mathero awo. Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera; Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke. Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa, amasesedwa kwathunthu ndi mantha! Monga loto pamene wina adzuka, kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye, mudzawanyoza ngati maloto chabe. (Masalimo 73:1-20)
Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma. (Miyambo 11:16)
Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse ndikati nditsutsane nanu. Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino? Inu munawadzala ndipo anamera mizu; amakula ndi kubereka zipatso. Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse, koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu. (Yeremiya 12:1-2)
Olemera osapembedza
Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000. (1 Samueli 25:2)
Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. (Estere 1:4)
Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. (Estere 5:11)
Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide; ndipo chuma chawo ndi chosatha. Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo; ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka. (Yesaya 2:7)
Pamene malonda ako ankawoloka nyanja unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu. Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako komanso ndi malonda ako. (Ezekieli 27:33)
“Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi. (Danieli 11:2)
Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. (Luka 19:2)
Lamulo losafunafuna kulemera kwa anthu ena
Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse. (Deuteronomo 23:6)
Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’ (Ezara 9:12)
Njira yolakwika yolemerera
Ena amalemera pochimwa popanda kuvomereza tchimo lawo
Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.” (Hoseya 12:8)
Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. (Zekariya 11:5)
Ena amadzionetsa ngati opembedza kuti alemere
Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.” (Oweruza 17:13)
Zina ndi zina
...ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika, (Miyambo 2:4)
Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena. (Mlaliki 10:20)
Nthawi zina anthu amanama za mmene chuma chawo chilili
Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse; munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri. (Miyambo 13:7)
Ndalama zimagwiritsidwa ntchito kuonetsa mtengo wa Ufumu wa Mulungu
“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo. “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.” (Mateyu 13:44-46)
Moyo wolungama ukufanizidwa ndi siliva
Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu. (Miyambo 10:20)
Chiweruzo pa mitundu yolemera yosapembedza
Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga, achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi. (Yesaya 15:7)
Inu muli ndi mitsinje yambiri ndi chuma chambiri. Koma chimaliziro chanu chafika, moyo wanu watha. (Yeremiya 51:13)
Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti, “Iwe Turo, umanena kuti, ‘Ndine wokongola kwambiri.’ “Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako. “Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako. “Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako. “Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo. “Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako. “Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako. “Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari. Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako. “Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo. “Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi. “Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako. “Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba. “Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali zonyamula malonda ako. Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi yodzaza ndi katundu wolemera. Anthu opalasa ako amakupititsa pa nyanja yozama. Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola pakati pa nyanja. Chuma chako, katundu wako, malonda ako, okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi, anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo adzamira mʼnyanja tsiku limene udzawonongeka. (Ezekieli 27:3, 12-27)
Israeli anali mpesa wotambalala; anabereka zipatso zambiri. Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka, anawonjezera kumanga maguwa ansembe. Pamene dziko lake linkatukuka, anakongoletsa miyala yake yopatulika. Mtima wawo ndi wonyenga ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Yehova adzagumula maguwa awo ansembe ndi kuwononga miyala yawo yopatulika. (Hoseya 10:1-2)
Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika; a malonda anu onse adzapululidwa, ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa. Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.” Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi. (Zefaniya 1:11, 13, 18)
Ndipo Turo anadzimangira linga; wadziwunjikira siliva ngati fumbi, ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu. Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja, ndipo adzapserera ndi moto. (Zekariya 9:3-4)
Mfumu sinkayenera kulemera mopitirira muyeso
Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.” Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri. (Deuteronomo 17:16-17)
Mafumu ananyalanyaza lamulo losalemera mopitirira muyeso
Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta. (1 Mafumu 4:26)
Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000, osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo. Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka. Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni. Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri. Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse. Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse. Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni. Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi. Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi. Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu. Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu. Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri. Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe. (1 Mafumu 10:14-28)
Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu. Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. Solomoni amagula akavalo ku Igupto ndi Kuwe pakuti anthu amalonda a mfumu amakawagula ku Kuwe. Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu. (2 Mbiri 1:14-17)
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.” Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni. (Anthu a Hiramu ndi anthu a Solomoni anabweretsa golide kuchokera ku Ofiri ndipo anabweretsanso mitengo ya mʼbawa ndi miyala yokongola. Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya mʼbawa pokonzera makwerero a Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndiponso kupangira anthu oyimba apangwe ndi azeze. Zinthu zonga zimenezi sizinaonekeponso mu Yuda). Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake. Kulemera kwa golide amene Solomoni amalandira pa chaka kunali makilogalamu 23,000, osawerengera amene ankabwera ndi anthu ochita malonda ndi osinthanitsa zinthu. Komanso mafumu onse a ku Arabiya ndi abwanamkubwa a mʼdzikomo amabweretsa golide ndi siliva kwa Solomoni. Mfumu Solomoni inapanga zishango zazikulu 200 zagolide wosasantha. Mʼchishango chilichonse mumalowa golide wolemera makilogalamu asanu ndi awiri. Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. Ndipo mfumu inapanganso mpando waukulu waufumu wa nyanga za njovu ndipo unakutidwa ndi golide woyengeka bwino. Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi ndi choyikapo mapazi cholumikizidwa ku mpandowo. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, ndi chifanizo cha mkango chitayima posanjikapo manjapo. Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi imodzi aja. Umodzi mbali ina ya khwerero ndi wina mbali inayo. Palibe mpando wonga uwu umene unapangidwapo mu ufumu wina uliwonse. Zikho zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndiponso zipangizo zonse za ku nyumba yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide oyengeka bwino. Panalibe chinthu chopangidwa ndi siliva, chifukwa siliva samayesedwa kanthu mʼnthawi ya Solomoni. Mfumu inali ndi sitima zambiri zapamadzi zimene zimayendetsedwa ndi antchito a Hiramu. Zimabwera kamodzi pa zaka zitatu zilizonse zitanyamula golide, siliva ndi nyanga za njovu, ndiponso anyani ndi apusi. Mfumu Solomoni anapambana mafumu ena onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu. Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo ndi magaleta, ndi akavalo 12,000 amene amawasunga mʼmizinda yosungira magaleta ndiponso ena anali ndi iye ku Yerusalemu. Iye ankalamulira mafumu onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika ku malire a dziko la Igupto. Mfumu inasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba mu Yerusalemu ndipo mikungudza kukhala yochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. (2 Mbiri 9:8-27)
Uneneri
Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso, amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako. (Masalimo 45:12)
Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse. Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?” Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.” Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse: Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. (Yesaya 39:2, 4-6)
Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe. Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova. Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali; patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi, zikubweretsa ana ako ochokera kutali, pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo, kudzalemekeza Yehova Mulungu wako, Woyerayo wa Israeli, pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero. Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse, sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku, kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo, akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo. (Yesaya 60:5-6, 9, 11)
Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova, adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu. Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira. Chifukwa manyazi awo anali owirikiza; ndi kuti munalandira chitonzo ndi kutukwana, adzakondwera ndi cholowa chawo, tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza, ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo. (Yesaya 61:6-7)
Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. (Hagai 2:7)
“Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ” (Zekariya 1:17)
Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’ ” (Zekariya 7:7)
Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri. Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa! (Chivumbulutso 6:15-16)
Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake. (Chivumbulutso 13:16-17)
Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. (Chivumbulutso 17:4)
Pakuti mayiko onse amwa vinyo ozunguza mutu wazigololo zake. Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo, ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.” (Chivumbulutso 18:3)
“Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo. “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro ndipo adzalira mokuwa kuti, “ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu, iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira, ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale! Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’ “Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti, “Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, kumene onse anali ndi sitima pa nyanja analemera kudzera mʼchuma chake! Mu ora limodzi wawonongedwa. (Chivumbulutso 18:11-19)
Chiyembekezo cha chuma chimagwiritsidwa ntchito kulimbikitsa
Khazikikani pakati pathu. Mukhoza kupeza malo wokhala kulikonse kumene mufuna. Mukhozanso kuchita malonda momasuka ndi kupeza chuma.” Pamenepo Sekemu anati kwa abambo ndi alongo ake a Dina, “Inu mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani chilichonse munganene. Tchulani mtengo wamalowolo umene ndiyenera kupereka, ndipo ndipereka. Ndidzakupatsani chilichonse chimene mukufuna malingana inu mukandipatsa namwaliyu kuti ndimukwatire.” (Genesis 34:10-12)
Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi. Tikatero, ndiye kuti ziweto zawo zonsezi, katundu wawo yenseyu ndi ziweto zawo zina zonsezi zidzakhala zathu. Choncho tiyeni tiwavomereze ndipo adzakhazikika pakati pathu.” (Genesis 34:21, 23)
Ndipo Aisraeli ankanena kuti, “Kodi mwamuona munthu akubwerayo? Iye amangobwera kudzanyoza Israeli. Tsono mfumu inati kuti idzapereka chuma chambiri kwa munthu amene adzamuphe. Idzaperekanso mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndiponso banja la abambo ake silidzaperekanso msonkho mu Israeli.” (1 Samueli 17:25)